Maliro 1:7 - Buku Lopatulika7 M'masiku a msauko wake ndi kusochera kwake Yerusalemu ukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire; pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa, mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 M'masiku a msauko wake ndi kusochera kwake Yerusalemu ukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire; pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa, mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Pa masiku a mavuto ake ndi a kuzunzika kwake, Yerusalemu amakumbukira zabwino zonse zimene anali nazo masiku amakedzana. Pamene anthu ake adagwa m'manja mwa adani, panalibe womuthandiza. Adani ake ankamupenyetsetsa monyodola namaseka kugwa kwake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Pa masiku a masautso ndi kuzunzika kwake, Yerusalemu amakumbukira chuma chonse chimene mʼmasiku amakedzana chinali chake. Anthu ake atagwidwa ndi adani ake, panalibe aliyense womuthandiza. Adani ake ankamuyangʼana ndi kumuseka chifukwa cha kuwonongeka kwake. Onani mutuwo |