Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 1:6 - Buku Lopatulika

6 Ulemu wake wonse wamchokera mwana wamkazi wa Ziyoni; akalonga ake asanduka nswala zosapeza busa, anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompirikitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ulemu wake wonse wamchokera mwana wamkazi wa Ziyoni; akalonga ake asanduka nswala zosapeza busa, anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompirikitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ulemerero wonse wa Ziyoni wachokeratu. Akalonga ake asanduka ngati mphoyo zosoŵa msipu. Ankathaŵa opanda ndi mphamvu zomwe, pofika adani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ulemerero wonse wa mwana wamkazi wa Ziyoni wachokeratu. Akalonga ake ali ngati mbawala zosowa msipu; alibe mphamvu zothawira owathamangitsa.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:6
31 Mawu Ofanana  

Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.


Pamenepo linga la mzindawo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamzinda pouzinga; nimuka mfumu panjira ya kuchidikha.


Koma nkhondo ya Ababiloni inalondola mfumu, nayipeza m'zidikha za Yeriko; koma nkhondo yake yonse inambalalikira.


Mulungu awalira mu Ziyoni, mokongola mwangwiro.


Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa, njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.


Mzinda wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.


Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.


Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni:


Pomveka migugu ya ziboda za olimba ake, pogumukira magaleta ake, ndi pophokosera njinga zake, atate sadzacheukira ana ao chifukwa cha kulefuka kwa manja ao;


Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.


Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, ndipo mfumu ya ku Babiloni inammanga m'zigologolo, nimtengera ku Babiloni, nimuika m'ndende mpaka tsiku la kufa kwake.


ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.


Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.


Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwachotsera mphamvu yao, chimwemwe chao chopambana, chowakonda m'maso mwao, ndi chokhumbitsa mtima wao, ana ao aamuna ndi aakazi,


Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa