Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 1:5 - Buku Lopatulika

5 Amaliwongo ake asanduka akulu ake, adani ake napindula; pakuti Yehova wamsautsa pochuluka zolakwa zake; ana ake aang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Amaliwongo ake asanduka akulu ake, adani ake napindula; pakuti Yehova wamsautsa pochuluka zolakwa zake; ana ake ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Adani ake asanduka omulamulira, odana naye akupeza bwino, popeza kuti Chauta wamugwetsa m'mavuto chifukwa cha machimo ochuluka a anthu ake. Ana ake amuchokera, atengedwa ukapolo ndi adani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Adani ake asanduka mabwana ake; odana naye akupeza bwino. Yehova wamubweretsera mavuto chifukwa cha machimo ake ambiri. Ana ake atengedwa ukapolo pamaso pa mdani.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:5
38 Mawu Ofanana  

popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao mu Ejipito, mpaka lero lino.


Mutiika kuti atilimbirane anzathu; ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha.


Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa; munakondweretsa adani ake onse.


Pakuti nditsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, lochokera kwa Ambuye, Yehova wa makamu, m'chigwa cha masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kufuulira kumapiri.


Anthu anu opatulika anakhala nacho kanthawi kokha; adani athu apondereza Kachisi wanu wopatulika.


Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga atuluka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kutchinga nsalu zanga.


Ndachoka kunyumba yanga, ndasiya cholowa changa; ndapereka wokondedwa wa mtima wanga m'dzanja la adani.


Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni.


Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?


Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.


Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.


Yerusalemu wachimwa kwambiri; chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa; onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche; inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.


Yehova wachita chomwe analingalira; watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale; wagwetsa osachitira chisoni; wakondweretsa adani pa iwe, wakweza nyanga ya amaliwongo ako.


Adani athu onse anatiyasamira.


Ndipo Inenso diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, koma ndidzawabwezera njira yao pamutu pao.


Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mzindawo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.


Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa