Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 1:12 - Buku Lopatulika

12 Kodi muyesa chimenechi chabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china ngati changachi amandimvetsa ine, chimene Yehova wandisautsa nacho tsiku la mkwiyo wake waukali?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Kodi muyesa chimenechi chabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china ngati changachi amandimvetsa ine, chimene Yehova wandisautsa nacho tsiku la mkwiyo wake waukali?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu amene mukudutsanu? Tangopenyani, muwone ngati pali mavuto ena onga angaŵa, mavuto amene Chauta adandigwetsamo, pamene adandikwiyira koopsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu nonse mukudutsa? Yangʼanani ndipo muone. Kodi pali mavuto ofanana ndi amene andigwerawa, amene Ambuye anandibweretsera pa tsiku la ukali wake?

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:12
18 Mawu Ofanana  

Kuzaza kwanu kwandimiza; zoopsa zanu zinandiononga.


Chifukwa chake ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kuchokera m'malo ake, m'mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wake waukali.


Tsoka ine, ndalaswa! Bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu vuto langa ndi ili, ndipirire nalo.


kuti aliyense dziko lao likhale lodabwitsa, ndi kutsonya chitsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wake.


Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, chatuluka, chimphepo chakukokolola: chidzagwa pamutu pa oipa.


Mkwiyo waukali wa Yehova sudzabwerera, mpaka wachita, mpaka watha zomwe afuna kuchita m'mtima mwake: masiku akumaliza mudzachizindikira.


Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.


Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerere pa ife.


Kodi sunaseke Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.


Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.


Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.


Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?


Ndipo anakwaniritsa mau ake adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera choipa chachikulu; pakuti pansi pa thambo lonse sipanachitike monga umo panachitikira Yerusalemu.


tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.


pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa