Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 1:11 - Buku Lopatulika

11 Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Anthu ake onse amabuula akamafunafuna chakudya. Chuma chao amagulitsana ndi chakudya, kuti apezenso mphamvu. Akuti, “Inu Chauta penyani, muwone m'mene akundinyozera.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Anthu ake onse akubuwula pamene akufunafuna chakudya; asinthanitsa chuma chawo ndi chakudya kuti akhale ndi moyo. “Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani, chifukwa ine ndanyozeka.”

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:11
20 Mawu Ofanana  

Koma mu Samariya munali njala yaikulu; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa bulu unagulidwa masekeli a siliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa kabu wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi masekeli asiliva asanu.


Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani? Ndigwira pakamwa.


Takhala chotonza cha anansi athu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.


Chifukwa chake atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa cha mtengo wake ndi chonyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo.


Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.


Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mzindamu.


Mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, njala inavuta m'mzinda, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya.


Yerusalemu wachimwa kwambiri; chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa; onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche; inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.


Udyo wake unali m'nsalu zake; sunakumbukire chitsiriziro chake; chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza; taonani, Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mzindawu, potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.


Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye?


Yehova, kumbukirani chotigwerachi, penyani nimuone chitonzo chathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa