Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 1:10 - Buku Lopatulika

10 Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Adani adamulanda chuma chake chonse. M'malo ake oyera mudaloŵa anthu a mitundu ina, amene Inu Chauta mudaŵaletsa kuloŵa mumsonkhano mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Adani amulanda chuma chake chonse; iye anaona mitundu ya anthu achikunja ikulowa mʼmalo ake opatulika, amene Inu Mulungu munawaletsa kulowa mu msonkhano wanu.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:10
22 Mawu Ofanana  

Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.


Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse;


Anthu anu opatulika anakhala nacho kanthawi kokha; adani athu apondereza Kachisi wanu wopatulika.


Chuma chako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wake, ichicho chidzakugwera chifukwa cha zochimwa zako zonse, m'malire ako onse.


Ndiponso ndidzapereka chuma chonse cha mzinda uwu, ndi zaphindu zake zonse, ndi zinthu zake zonse za mtengo wake, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babiloni.


Pakuti Yehova wa makamu atero, za zoimiritsa, ndi za thawale, ndi za zoikirapo, ndi za zipangizo zotsala m'mzinda uwu,


inde, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu;


Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babiloni, kuti alalikire mu Ziyoni kubwezera chilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.


Tili ndi manyazi, chifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m'malo opatulika a nyumba ya Yehova.


ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.


M'masiku a msauko wake ndi kusochera kwake Yerusalemu ukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire; pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa, mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake.


popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.


Ndipo nkhope yanga idzawayang'anira kumbali, ndipo iwo adzadetsa pobisika panga, nadzalowamo achifwamba, nadzamudetsa.


Nati kwa iwo, Muipse nyumbayi ndi kudzaza mabwalo ndi ophedwa, mukani. Ndipo anatuluka, nakantha m'mzindamo.


Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:


Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;


popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa