Malaki 3:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Ndidzaletsa tizilombo kuti tisadye mbeu zanu, mipesa yanu sidzaleka kubala. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Onani mutuwo |