Malaki 2:17 - Buku Lopatulika17 Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Mwatopetsa Chauta ndi zolankhula zanu. Komabe mumati, “Kodi tamtopetsa bwanji?” Mwamtopetsa ponena kuti, “Aliyense wochita zoipa ndi wabwino pamaso pa Chauta, ndipo Iye amakondwera naye.” Kapenanso pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wochita zolungamayo?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Mwamutopetsa Yehova ndi zoyankhula zanu. Inu mukufunsa kuti, “Kodi tamutopetsa bwanji?” Mwamutopetsa ponena kuti, “Aliyense amene amachita zoyipa ndi wabwino pamaso pa Yehova ndipo iye amakondwera naye” kapena pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu woweruza mwachilungamo?” Onani mutuwo |