Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:43 - Buku Lopatulika

43 Ndipo kunali, kuti anakhala iye mu Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Tsono Petro adakhala ku Yopa masiku ambiri kwa munthu wina, dzina lake Simoni, mmisiri wa zikopa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Petro anakhala ku Yopa kwa masiku ambiri kwa munthu wina, dzina lake Simoni, mmisiri wa zikopa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:43
12 Mawu Ofanana  

ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.


Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja.


Ndipo tsopano tumiza amuna ku Yopa, aitane munthu Simoni, wotchedwanso Petro;


acherezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja.


ndipo m'mene adawafotokozera zonse, anawatuma ku Yopa.


ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m'nyumba yake, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro;


Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja.


Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.


Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.


ndi Meyarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pa Yopa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa