Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo Petro ananyamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye kuchipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo Petro ananyamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye kuchipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Tsono Petro adanyamuka napita nawo. Pamene iye adafika, adamperekeza ku chipinda cham'mwamba chija. Akazi onse amasiye adangoti kwete m'mbali mwakemu, akungolira, nkumamuwonetsa malaya ndi zovala zina zimene Dorika ankasoka ali nawo pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Petro ananyamuka, napita nawo, ndipo atafika anamutengera ku chipinda chammwamba. Amasiye onse anayima momuzungulira akulira ndi kumuonetsa mwinjiro ndi zovala zina zimene Dorika ankapanga akanali moyo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:39
26 Mawu Ofanana  

Ana aakazi inu a Israele, mulirire Saulo, amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa, amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu.


Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno.


Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.


Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.


M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.


Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.


Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro aakulu.


Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.


ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;


Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.


Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.


Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.


Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa