Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:26 - Buku Lopatulika

26 Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Saulo atafika ku Yerusalemu, adayesa kuloŵa m'gulu la ophunzira aja. Koma onse adachita naye mantha, osakhulupirira kuti nayenso ndi wophunzira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Saulo atafika ku Yerusalemu, anayesetsa kulowa mʼgulu la ophunzira koma onse anamuopa chifukwa sanakhulupirire kuti anali wophunziradi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:26
9 Mawu Ofanana  

Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.


komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.


Ndipo m'mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza zilizonse ansembe aakulu ndi akulu adanena nao.


ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu. Ndipo anakhala pamodzi ndi ophunzira a ku Damasiko masiku ena.


koma ophunzira ake anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa mu dengu.


ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa