Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:22 - Buku Lopatulika

22 Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala mu Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m'Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Tsono mphamvu za Saulo zinkakulirakulira, ndipo adathetsa nzeru Ayuda okhala ku Damasiko pakuŵatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Koma mphamvu za Saulo zinali kukulirakulira ndipo anathetsa nzeru Ayuda okhala ku Damasiko powatsimikizira kuti Yesu ndi Mpulumutsi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:22
21 Mawu Ofanana  

Koma uta wake unakhala wamphamvu, ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa. Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo. (Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele.)


Koma wolungama asungitsa njira yake, ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.


Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.


Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu, aoneka pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.


Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.


Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.


Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga mu Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu.


Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye;


Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti mu Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.


koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu;


Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa