Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga mu Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga m'Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Anthu onse amene ankamva mau akewo ankadabwa, namafunsana kuti, “Kodi ameneyu si yemwe uja amene ku Yerusalemu ankapha anthu otama dzinali mopemba? Kodi siwabwera kuno kuti aŵamange otereŵa ndi kukaŵapereka kwa akulu a ansembe?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Onse amene anamva iye akulalikira anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene anayambitsa kuzunza okhulupirira ku mpingo wa ku Yerusalemu? Kodi siwabwera kuno kuti awamange ndi kuwapereka kwa akulu a ansembe?”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:21
20 Mawu Ofanana  

Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.


Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri; koma Inu ndinu pothawira panga polimba.


Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.


Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.


Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo, kapena ula mwa Israele; pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele, chimene Mulungu achita.


Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani?


Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'chilankhulidwe chake cha iye yekha.


namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Chipata Chokongola cha Kachisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera.


Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala mu Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu.


pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake, ndi kukhala wodabwizitsa mwa onse akukhulupirira (popeza munakhulupirira umboni wathu wa kwa inu) m'tsiku lija.


Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa