Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:19 - Buku Lopatulika

19 ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu. Ndipo anakhala pamodzi ndi ophunzira a ku Damasiko masiku ena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu. Ndipo anakhala pamodzi ndi ophunzira a ku Damasiko masiku ena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 ndipo atadya chakudya, adapezanso mphamvu. Saulo adakhala masiku angapo limodzi ndi ophunzira a ku Damasiko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 ndipo atadya chakudya, anapezanso mphamvu. Saulo anakhala masiku angapo ndi ophunzira a ku Damasiko.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:19
11 Mawu Ofanana  

Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.


ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya.


Ndipo ophunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala mu Yudeya;


komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.


Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m'maso mwake ngati mamba, ndipo anapenyanso; ndipo ananyamuka nabatizidwa;


Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.


Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife.


kapena kukwera kunka ku Yerusalemu sindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.


nampatsanso chigamphu cha nchinchi ya nkhuyu ndi nchinchi ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wake unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya chakudya, osamwa madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa