Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Ananiya anayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu mu Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Ananiya anayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Atamva zimenezo Ananiya adati, “Ambuye, anthu ambiri andiwuza za munthu ameneyu, kuti adaŵachita zoipa zambiri anthu anu ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Hananiya anayankha kuti, “Ambuye, ndinamva zambiri za munthu uyu ndi zonse zoyipa anachitira oyera mtima a ku Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:13
31 Mawu Ofanana  

M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,


Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga mu Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu.


Koma kunali, pakupita Petro ponseponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhala ku Lida.


Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.


kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.


kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;


Moni kwa Filologo ndi Juliya, Nereo ndi mlongo wake, ndi Olimpasi, ndi oyera mtima onse ali pamodzi nao.


kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.


kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala mu Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:


pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.


Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.


Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,


Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali mu Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:


Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:


Oyera mtima onse akupatsani inu moni, koma makamaka iwo a banja la Kaisara.


kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a mu Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu.


Perekani moni kwa atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Akupatsani moni iwo a ku Italiya.


Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.


Ndipo Samuele anati, Ndikamuka bwanji? Saulo akachimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa