Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yudasi ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yudasi ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Apo Ambuye adamuuza kuti, “Nyamuka, upite ku mseu wa mumzindamu umene amati, ‘Njira Yolunjika.’ Ndipo ku nyumba ya Yudasi ukafune munthu wina wa ku Tariso, dzina lake Saulo. Panopa akupemphera,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ambuye anamuwuza iye kuti, “Nyamuka, pita ku nyumba ya Yudasi imene ili pa Njira Yolunjika ndipo ukafunse za munthu wochokera ku Tarisisi dzina lake Saulo, pakuti akupemphera.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:11
28 Mawu Ofanana  

Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.


ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m'nyumba yake, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro;


Ndipo anatuluka kunka ku Tariso kufunafuna Saulo;


Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.


Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa mu Silisiya, mfulu ya mzinda womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu.


Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;


Chifukwa chake lapa choipa chako ichi, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe cholingirira cha mtima wako.


Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.


Koma m'mene abale anachidziwa, anapita naye ku Kesareya, namtumiza achokeko kunka ku Tariso.


Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa