Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:32 - Buku Lopatulika

32 Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegule pakamwa pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegula pakamwa pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Mau a m'Malembo amene ankaŵerengawo ndi aŵa: “Iye anali ngati nkhosa yoitsogoza pokaipha, ngati mwana wankhosa wongokhala duu pomumeta. Sadalankhulepo kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa: “Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:32
18 Mawu Ofanana  

Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala chete osalawa chokoma; ndipo chisoni changa chinabuka.


Ndinakhala duu, sindinatsegule pakamwa panga; chifukwa inu mudachichita.


Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwe kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye padziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.


Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.


Ndidzawagwetsa kuti aphedwe monga anaankhosa amphongo, ndi atonde.


ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;


ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;


Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.


M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.


Monganso kwalembedwa, Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha.


Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Khristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo;


koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa