Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:31 - Buku Lopatulika

31 Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Iye adati, “Ha, ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Motero adaitana Filipo kuti adzakwere ndi kukhala naye pagaletapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Iye anayankha kuti, “Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Ndipo iye anayitana Filipo kuti abwere ndikukhala naye mʼgaleta.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:31
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeze kodi, umo munthuyo anatembenuka pa galeta wake kukomana ndi iwe? Kodi nyengo ino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zovala, ndi minda ya azitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo, ndi adzakazi?


M'mwemo Naamani anadza ndi akavalo ake ndi magaleta ake, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa.


ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu.


Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasochera m'menemo.


Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.


Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga?


Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegule pakamwa pake.


Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?


Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.


Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa.


ndipo mbale wolemera anyadire pamene atsitsidwa, pakuti adzapita monga duwa la udzu.


Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa