Machitidwe a Atumwi 8:27 - Buku Lopatulika27 Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Filipo adanyamukadi napita. Ndipo munthu wina wa ku Etiopiya adaabwera ku Yerusalemu kudzapembedza. Iyeyu anali nduna yaikulu ya m'banja la mfumukazi Kandake wa ku Etiopiya, ndiponso woyang'anira chuma chake chonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Ndipo ananyamuka napita, ndipo akuyenda anakumana ndi munthu wa ku Etiopia wa udindo waukulu woyangʼanira chuma cha Kandake, mfumu yayikazi ya ku Etiopia. Munthu ameneyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu, Onani mutuwo |
Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.