Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:25 - Buku Lopatulika

25 Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwera kunka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino kumidzi yambiri ya Asamariya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwera kunka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino kumidzi yambiri ya Asamariya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Petro ndi Yohane atatha kupereka umboni wao ndi kulalika mau a Ambuye, adabwerera ku Yerusalemu. Ankapita nalalika Uthenga Wabwino m'midzi yambiri ya Asamariya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Atatha kuchitira umboni ndi kulalikira mawu a Ambuye, Petro ndi Yohane anabwerera ku Yerusalemu, atalalikira Uthenga Wabwino mʼmidzi yambiri ya Asamariya.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:25
14 Mawu Ofanana  

Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:


pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo.


Ndipo inunso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi.


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Pamenepo kazembe, pakuona chochitikacho anakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye.


Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.


ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.


Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.


Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa