Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:60 - Buku Lopatulika

60 Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau aakulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

60 Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau akulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

60 Ndipo adagwada pansi nafuula kwakukulu kuti, “Ambuye, musaŵaŵerengere tchimoli.” Atanena mau ameneŵa, adafa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

60 Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:60
23 Mawu Ofanana  

Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, chovala changa ndi malaya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;


Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.


Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.


ndi manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka;


koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu;


Ndipo anapatukana nao kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera,


Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.


dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.


Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.


Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;


Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.


Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,


Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.


Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona.


Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu anatayika.


Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choyamba cha iwo akugona.


Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,


pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;


amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.


Pa chodzikanira changa choyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; chimenecho chisawerengedwe chowatsutsa.


ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa