Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:56 - Buku Lopatulika

56 nati, Taonani, ndipenya mu Mwamba motseguka, ndi Mwana wa Munthu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

56 nati, Taonani, ndipenya m'Mwamba motseguka, ndi Mwana wa Munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

56 Tsono adati, “Onani! Ndikuwona Kumwamba kotsekuka, ndipo Mwana wa Munthu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

56 Stefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:56
17 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.


Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:


Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:


Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,


Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa Munthu.


ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi chotengera chilinkutsika, chonga ngati chinsalu chachikulu, chogwiridwa pangodya zake zinai, ndi kutsikira padziko pansi;


Ndipo chinachitika katatu ichi; ndipo pomwepo chotengeracho chinatengedwa kunka kumwamba.


Koma anafuula ndi mau aakulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;


Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.


Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.


Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka mu Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m'tsogolomo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa