Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:48 - Buku Lopatulika

48 Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

48 Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

48 Ngakhale zinali choncho Mulungu Wopambanazonse sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja, monga akunenera mneneri kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

48 “Komatu, Wammwambamwambayo sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi anthu. Monga mneneri akunena kuti,

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:48
17 Mawu Ofanana  

Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.


Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?


Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.


Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga! Udaika Wam'mwambamwamba chokhalamo chako;


Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse.


Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.


Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;


Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.


Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake:


Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.


Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa