Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:42 - Buku Lopatulika

42 Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri, Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri, Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Pamenepo Mulungu adaŵafulatira, naŵapereka ku machimo akupembedza nyenyezi, monga akunenera mau olembedwa m'buku la aneneri kuti, “ ‘Inu Aisraele, musayese kuti munkapereka kwa Ine nyama zimene munkapha ndi kuzipereka ngati nsembe pa zaka makumi anai zija m'chipululu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Koma Mulungu anawafulatira, nawapereka kuti apembedze zolengedwa zakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la aneneri kuti, “ ‘Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?’

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:42
26 Mawu Ofanana  

Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.


Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.


Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.


Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritse ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi lubani.


Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.


Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamve konse; koma anachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene sindinakondwere nacho.


ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.


ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.


Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo;


Ndipo inu, nyumba ya Israele, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ake, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvere Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.


Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa.


Efuremu waphatikana ndi mafano, mlekeni.


Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.


Chifukwa chake penyerani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo:


Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.


nakatumikira milungu ina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;


ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.


chimene makolo anu anandiyesa nacho, ndi kundivomereza, naona ntchito zanga zaka makumi anai.


Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yachilendo, adzatembenuka ndi kukuchitirani choipa, ndi kukuthani, angakhale anakuchitirani chokoma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa