Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:36 - Buku Lopatulika

36 Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro mu Ejipito, ndi mu Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro m'Ejipito, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Moseyo ndiye adaŵatsogolera anthuwo naŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ankachita zozizwitsa ndi zizindikiro ku Ejipito, pa Nyanja Yofiira, ndiponso m'chipululu zaka makumi anai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Iye anawatulutsa mu Igupto ndipo anachita zodabwitsa ndi zizindikiro zozizwitsa mu Igupto, pa Nyanja Yofiira, ndiponso mʼchipululu kwa zaka makumi anayi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:36
38 Mawu Ofanana  

nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.


Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.


Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba, ngati tsiku la ku Masa m'chipululu.


Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m'dziko la Ejipito.


Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.


Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.


Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;


Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.


Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'chipululu.


Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri, Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu?


Zovala zanu sizinathe pathupi panu, phazi lanu silinatupe zaka izi makumi anai.


musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo, monga muja tsiku la chiyesero m'chipululu,


chimene makolo anu anandiyesa nacho, ndi kundivomereza, naona ntchito zanga zaka makumi anai.


losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao, tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuluke m'dziko la Ejipito; kuti iwo sanakhalebe m'pangano langa, ndipo Ine sindinawasamalire iwo, anena Ambuye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa