Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 6:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu a milandu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Motero adautsa mitima ya anthu, ya akuluakulu ao, ndiponso ya aphunzitsi a Malamulo. Iwoŵa adamuukira Stefano, namgwira, nkupita naye ku Bungwe Lalikulu la Ayuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Motero anawutsa mitima ya anthu, akulu ndi aphunzitsi amalamulo. Anamugwira Stefano ndi kumubweretsa ku Bwalo Lalikulu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 6:12
15 Mawu Ofanana  

Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.


Ndipo iwo akugwira Yesu ananka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Ndipo kunali lina la masiku ao m'mene Iye analikuphunzitsa anthu mu Kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe aakulu ndi alembi pamodzi ndi akulu;


Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao.


Koma Ayuda osamvera anautsa mitima ya Agriki kuti aipse abale athu.


Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereanso, anadza komwekonso, nautsa, navuta makamu.


Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro,


Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye mu Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,


nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba.


Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pabwalo la akulu a milandu. Ndipo anawafunsa mkulu wa ansembe,


Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa