Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:40 - Buku Lopatulika

40 Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Abwalowo adavomerezana naye, naŵaitana atumwi aja. Adaŵakwapula, naŵaletsa kuti asalankhulenso m'dzina la Yesu, kenaka adaŵalola kuti apite.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Akuluakulu enawo anavomerezana naye. Iwo anayitana atumwi aja ndipo anawakwapula kwambiri. Ndipo anawalamula kuti asayankhulenso mʼdzina la Yesu ndipo anawamasula.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:40
13 Mawu Ofanana  

Wolungama asamalira moyo wa choweta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza.


amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;


Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.


Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka.


Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao;


nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.


Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;


Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.


Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu.


nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.


Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa