Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:38 - Buku Lopatulika

38 Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Nchifukwa chake pa nkhani imeneyi ndikukuuzani kuti, muŵaleke anthuŵa, ndipo muŵalole azipita. Ngati zimene iwo akuganiza ndiponso zimene akuchitazi nzochokera kwa anthu, zidzakanika zokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Chifukwa chake pa nkhani iyi ndikuwuzani kuti, alekeni anthuwa ndipo aloleni apite! Pakuti ngati zimene akuganiza kapena kuchita ndi zochokera kwa munthu zidzalephera.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:38
14 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


kuti Ine ndidzathyola Aasiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphewa pao.


Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi, ngati Ambuye salamulira?


Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa.


Ubatizo wa Yohane uchokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? Mundiyankhe.


Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.


Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire.


Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa