Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:36 - Buku Lopatulika

36 Pakuti asanafike masiku ano anauka Teudasi, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, chiwerengero chao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pachabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Pakuti asanafike masiku ano anauka Teudasi, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, chiwerengero chao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pachabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Pajatu si kale pamene munthu wina dzina lake Teudasi adaabwera nkuyesa kudzimveketsa, ndipo anthu ngati mazana anai adamtsata. Iye uja adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana natheratu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Pakuti masiku a mʼmbuyomu kunali Teuda amene anadzitchukitsa, ndipo anthu pafupifupi 400 anamutsatira. Iye anaphedwa ndipo omutsatira akewo anabalalitsidwa, zonse zinatheratu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:36
14 Mawu Ofanana  

chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


Onani, Iye ali m'chipululu; musamukeko. Onani, ali m'zipinda; musavomereze.


Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.


Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu?


Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire.


Koma panali munthu dzina lake Simoni amene adachita matsenga m'mzindamo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkulu;


Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezere ine kanthu;


Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.


Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;


Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.


Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.


Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.


ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa