Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:28 - Buku Lopatulika

28 nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Adati, “Paja tidakuletsani mwamphamvu kuti musaphunzitse konse m'dzina la Yesu, koma inu mwafalitsa zophunzitsa zanuzo m'Yerusalemu monse, ndipo mukufuna kusenzetsa ife imfa ya munthu ameneyu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Iye anati, “Ife tinakuletsani kuti musaphunzitsenso mʼdzina ili, koma inu mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mukufuna kutisenzetsa imfa ya munthu ameneyu.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:28
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.


Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.


Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mzinda uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu.


Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.


Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silingathe kulola mau ake onse.


Ndipo iye wakugwa pamwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye.


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.


Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa