Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pabwalo la akulu a milandu. Ndipo anawafunsa mkulu wa ansembe,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pa bwalo la akulu. Ndipo anawafunsa mkulu wa ansembe,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Atafika nawo, adaŵakhazika pamaso pa Bungwe Lalikulu lija, ndipo mkulu wa ansembe onse adayamba kuŵafunsa mafunso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Atafika nawo atumwi aja, anawayimika pamaso pa Bwalo Lalikulu kuti afunsidwe mafunso ndi mkulu wa ansembe.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:27
8 Mawu Ofanana  

koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao,


Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu a milandu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.


Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu?


Ndipo atamva ichi, analowa mu Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu a milandu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.


Koma ananyamukapo wina pabwalo la akulu a milandu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa malamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.


Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu a milandu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa