Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:26 - Buku Lopatulika

26 Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Pamenepo mkulu wa asilikali uja pamodzi ndi asilikaliwo adapita nkukaŵatenga atumwiwo. Sadaŵatenge mwankhondo ai, chifukwa ankaopa kuti anthu angaŵaponye miyala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Pamenepo mkulu wa alonda pamodzi ndi alonda anakawatenga atumwi. Sanakawatenge mwaukali, chifukwa amaopa kuti anthu angawaponye miyala.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:26
13 Mawu Ofanana  

Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri.


Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.


Koma ananena iwo, pa nthawi ya chikondwerero iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.


Koma Petro anamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone chimaliziro.


Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.


Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.


Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna maphedwe ake pakuti anaopa anthuwo.


Ndipo iye anachoka, nalankhulana ndi ansembe aakulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo.


Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.


Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;


Koma anyamata amene adafikako sanawapeze m'ndende, ndipo pobwera anafotokoza,


Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani.


Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali mu Kachisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa