Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:24 - Buku Lopatulika

24 Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Pamene mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe adamva mau ameneŵa, adatha nawo nzeru, osadziŵa kwachitika zotani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Mkulu wa alonda a Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe atamva zimenezi anathedwa nzeru, osadziwa kuti zimenezi zidzatha bwanji.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:24
17 Mawu Ofanana  

Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


Ndipo iye anachoka, nalankhulana ndi ansembe aakulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo.


Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba?


Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.


Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani?


Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa ku Kachisi ndi Asaduki anadzako,


Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.


nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.


Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali mu Kachisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.


Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa