Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:22 - Buku Lopatulika

22 Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Ndipo munthu wochiritsidwa mododometsayo anali wa zaka zopitirira makumi anai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ndipo munthu amene anachiritsidwayo anali ndi zaka makumi anayi.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:22
8 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;


Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.


Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.


Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona chibadwire.


Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa mu Kachisi;


Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.


Ndipo m'mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza zilizonse ansembe aakulu ndi akulu adanena nao.


Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa