Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipotu pakuona munthu wochiritsidwayo alikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipotu pakuona munthu wochiritsidwayo alikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tsono poonanso munthu wochiritsidwa uja ataimirira pafupi ndi Petro ndi Yohane, adasoŵa poŵatsutsira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma popeza iwo amamuona munthu amene anachiritsidwa atayima pamodzi ndi iwo, palibe chimene akananena.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:14
7 Mawu Ofanana  

Popeza tsono izi sizikanika, muyenera inu kukhala chete, ndi kusachita kanthu kaliuma.


zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


Koma pamene anawalamulira iwo achoke m'bwalo la akulu a milandu, ananena wina ndi mnzake,


kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chaoneka kwa onse akukhala mu Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.


Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa