Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 3:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo kudzali, kuti wamoyo aliyense samvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo kudzali, kuti wamoyo aliyense samvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Aliyense amene sadzamvera Mneneriyo, amchotseretu mwa Aisraele ndi kumuwononga.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Aliyense amene sadzamvera mawu a mneneriyo, adzayenera kuchotsedwa pakati pa abale ake.’

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 3:23
15 Mawu Ofanana  

Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake.


Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.


Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.


Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.


Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.


Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa.


Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.


Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;


tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;


Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.


Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa