Machitidwe a Atumwi 28:6 - Buku Lopatulika6 Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sanapweteke konse, anasintha maganizo, nati, Ndiye Mulungu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sikunampweteka, anapindula, nati, Ndiye Mulungu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Anthu aja ankayembekeza kuti thupi lake litupa, kapena kuti agwa mwadzidzidzi nkufa. Adakhala akumuyang'ana nthaŵi yaitali, koma ataona kuti palibe chilichonse chachilendo chimene chamchitikira, adasintha maganizo nati, “Ameneyu ndi mmodzi wa milungu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu. Onani mutuwo |