Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 27:43 - Buku Lopatulika

43 Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m'nyanja, nafike pamtunda,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m'nyanja, nafike pamtunda,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Koma mtsogoleri wa asilikali uja adafuna kupulumutsa Paulo, motero adaŵaletsa. Adalamula kuti onse otha kusambira, adziponye m'madzi, asambire kuti akafike ku mtunda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Koma wolamulira asilikali uja anafuna kupulumutsa Paulo ndipo anawaletsa kuchita zimene anakonza. Iye analamulira asilikali kuti amene amatha kusambira kuti adziponye mʼmadzi ndi kuyamba kukafika pa mtunda.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 27:43
8 Mawu Ofanana  

Njira za munthu zikakonda Yehova ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.


Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.


ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felikisi kazembeyo.


Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo.


Ndipo m'mawa mwake tinangokocheza ku Sidoni; ndipo Julio anachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze.


Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikali, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka.


Ndipo uphungu wa asilikali udati awaphe andende, angasambire, ndi kuthawa.


Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa