Machitidwe a Atumwi 27:41 - Buku Lopatulika41 Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201441 Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa41 Koma chombo chija chidakatsakamira pa mchenga wobisika ndi madzi, ndipo chidaima. Mbali yakutsogolo ya chombocho idajima, kotero kuti sichidathe kuyendanso. Ndipo mbali yakumbuyo idaonongeka ndi mphamvu ya mafunde. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero41 Koma sitimayo inagunda mchenga wobisika ndipo inayima. Mbali ya kutsogolo ya sitimayo inakanirira ndipo sinathe kuyendanso, ndipo mbali yakumbuyo inasweka ndi kuwomba kwa mafunde. Onani mutuwo |