Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 27:40 - Buku Lopatulika

40 Ndipo m'mene anataya anangula anawasiya m'nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikulu, analunjikitsa kumchenga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Ndipo m'mene anataya anangula anawasiya m'nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikulu, analunjikitsa kumchenga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Choncho adataya anangula naŵasiya m'nyanja. Nthaŵi yomweyo adamasula zingwe zomangira nkhafi zoongolera, nakweza thanga lakutsogolo, kuti mphepo ikankhe chombo, ndipo adalunjika ku mtunda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Atadula anangula aja, nawasiya mʼnyanja, pa nthawi yomweyo anamasula zingwe zimene anamangira zowongolera sitimayo. Kenaka anayimika chinsalu chimene mphepo imakankha kuti sitima iyende, ndipo anayamba kupita ku gombe.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 27:40
5 Mawu Ofanana  

Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wake, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo cholanda chachikulu, chofunkha chinagawanidwa; wopunduka nafumfula.


Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.


ndipo m'mene adaukweza, anachita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Siriti, anatsitsa matanga, natengedwa motero.


Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa