Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 27:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo m'mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalire masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng'ono anatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuke chidatichokera pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo m'mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalira masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng'ono anatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuke chidatichokera pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Sitidaone dzuŵa kapena nyenyezi masiku ambiri, koma namondwe ankakalipabe, mpaka tonse tidaatayiratu chikhulupiriro chakuti tipulumuka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Sitinaone dzuwa kapena nyenyezi kwa masiku ambiri ndipo namondwe anapitirira kuwomba kwambiri, pomaliza ife tonse tinalibenso chiyembekezo choti nʼkupulumuka.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 27:20
15 Mawu Ofanana  

Anatumiza mdima ndipo kunada; ndipo sanapikisane nao mau ake.


Unatopa ndi njira yako yaitali; koma sunanene, Palibe chiyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; chifukwa chake sunalefuke.


Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.


Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israele; taonani, akuti, Mafupa athu auma, chiyembekezo chathu chatayika, talikhidwa.


Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka.


Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka:


ndipo tsiku lachitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa.


Ndipo pamene atakhala nthawi yaikulu osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.


Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;


kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.


Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa