Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 27:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo poomba pang'ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo poomba pang'ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mphepo yakumwera itayamba kuwomba monyengerera, anthu aja adayesa kuti tsopano apeza mpata woti achite zimene ankafuna. Motero adanyamuka ulendo, nayenda m'mbali mwa chilumba chija cha Krete.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mphepo yochokera kummwera itayamba kuwomba pangʼonopangʼono, anthuwo anaganiza kuti apeza chimene amafuna; kotero analowetsa nangula ndipo anayamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba cha Krete.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 27:13
10 Mawu Ofanana  

Kodi mudziwa umo zovala zanu zifundira, pamene dziko lili thuu chifukwa cha mwera?


Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa, natsogoza mwera ndi mphamvu yake.


Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kumwera; nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zake zitulukemo. Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwake, nadye zipatso zake zofunika.


Ndipo pamene mphepo ya kumwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.


ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikulu za Mulungu.


Ndipo popeza dooko silinakome kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera.


Ndipo pamene atakhala nthawi yaikulu osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene.


ndipo popazapazapo movutika, tinafika kumalo ena dzina lake Pokocheza Pokoma; pafupi pamenepo panali mzinda wa Lasea.


Wina wa mwa iwo, ndiye mneneri wa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zilombo zoipa, aumbombo, aulesi.


Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe mu Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa