Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 27:10 - Buku Lopatulika

10 nanena nao, Amuna inu, ndiona ine kuti ulendo udzatitengera kuonongeka ndi kutayika kwambiri, si kwa akatundu okha kapena ngalawa yokha, komatunso kwa moyo wathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 nanena nao, Amuna inu, ndiona ine kuti ulendo udzatitengera kuonongeka ndi kutayika kwambiri, si kwa akatundu okha kapena ngalawa yokha, komatunso kwa moyo wathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Abale, ine ndikuwona kuti pa ulendowu zinthu zambiri zidzawonongeka ndi kutayika, osati katundu yekha ndi chombo ai, komanso moyo wathu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Anthu inu, ine ndikuona kuti ulendo wathuwu ukhala woopsa ndipo katundu ndi sitima ziwonongeka, ngakhalenso miyoyo yathu.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 27:10
12 Mawu Ofanana  

Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye; ndipo adzawadziwitsa pangano lake.


Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwe kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.


Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.


Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kipro, tinachisiya kulamanzere, nkupita ku Siriya; ndipo tinakocheza ku Tiro; pakuti pamenepo ngalawa inafuna kutula akatundu ake.


Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikali, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka.


Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pamutu wa mmodzi wa inu.


Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa