Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 26:13 - Buku Lopatulika

13 dzuwa lamsana, ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kochokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 dzuwa lamsana, ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kochokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pa njira, nthaŵi yamasana dzuŵa lili pa mutu, inu amfumu, ndidaona kuŵala kochokera kumwamba. Kuŵalako kunali koposa kuŵala kwa dzuŵa, ndipo kudatizinga tonse, ine ndi anzanga aulendo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Wolemekezeka Mfumu, nthawi ya masana pamene ndimayenda pa msewu, ndinaona kuwala kuchokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa kutandizungulira ine pamodzi ndi anzangawo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 26:13
10 Mawu Ofanana  

Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi mu Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.


Komanso kuwala kwake kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ake, nadzapoletsa chilonda chimene anawakantha ena.


ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.


Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba.


Ndipo iwo akukhala nane anaonadi kuunika, koma sanamve mau akulankhula nane.


M'menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe aakulu,


Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira.


Ndipo poyenda ulendo wake, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kochokera kumwamba;


Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.


Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa