Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 24:22 - Buku Lopatulika

22 Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Felikisi ankadziŵa bwino za Njira ya Ambuye, choncho adatseka bwalolo ndi mau akuti, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera Lisiasi, mkulu wa asilikali.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Kenaka Felike, amene amadziwa bwino za Njirayo, anayamba wayimitsa mlanduwo, nati, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera mkulu wa asilikali Lusiya.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 24:22
11 Mawu Ofanana  

Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m'tseri, nafunsitsa iwo nthawi yake idaoneka nyenyeziyo.


Pamene iwo anamfunsa iye kuti akhale nthawi ina yoenjezerapo, sanavomereze;


Pakutinso palipo potiopsa kuti adzatineneza za chipolowe chalero; popeza palibe chifukwa cha kufotokozera za chipiringu chimene.


Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;


Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri;


Koma atapita masiku ena, anadza Felikisi ndi Durusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro cha Khristu Yesu.


amenenso anayesa kuipsa Kachisi; amene tamgwira.


Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.


makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.


napempha kwa iye makalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.


ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa