Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 24:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 “Tsono nditakhala kwina zaka zingapo, ndidabwera kudzatula zopereka zachifundo kwa anthu a mtundu wanga, ndiponso kudzapereka nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “Patapita zaka zambiri, ndinabwera ku Yerusalemu kudzapereka mphatso kwa anthu osauka a mtundu wanga komanso kudzapereka nsembe.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 24:17
14 Mawu Ofanana  

Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi mu Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste.


Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleke usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi.


Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwake m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa mu Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.


Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; chifukwa chakenso anamuitana iye kawirikawiri, nakamba naye.


kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;


Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.


Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.


Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;


pokhapo kuti tikumbukire aumphawi; ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa