Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 24:12 - Buku Lopatulika

12 ndipo sanandipeze mu Kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m'sunagoge kapena m'mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 ndipo sanandipeza m'Kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m'sunagoge kapena m'mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ayuda sadandipezepo ndikukangana ndi munthu aliyense m'Nyumba ya Mulungu, kapena kuutsa chipolowe pakati pa anthu m'nyumba zamapemphero, kaya pena paliponse mumzindamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Amene akundiyimba mlanduwa sanandipeze mʼNyumba ya Mulungu ndi kutsutsana ndi wina aliyense kapena kuyambitsa chisokonezo mʼsunagoge kapena pena paliponse mu mzindamo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 24:12
6 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikulu la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.


Undifunsiranji Ine? Funsa iwo amene adamva chimene ndinalankhula nao; taona, amenewo adziwa chimene ndinanena Ine.


popereka izi anandipeza woyeretsedwa mu Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso;


Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;


koma Paulo podzikanira ananena, Sindinachimwe kanthu kapena pachilamulo cha Chiyuda, kapena pa Kachisi, kapena pa Kaisara.


Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachite kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa