Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 24:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Bwanamkubwa uja adakodola Paulo kuti alankhule, ndipo Paulo adati, “Ndikudziŵa kuti inu mwakhala mukuweruza mtundu uwu zaka zambiri tsopano, nchifukwa chake ndakondwa kuti ndiyankhe pamaso panu zimene akundinenezazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Bwanamkubwayo atakodola Paulo ndi kulola kuti ayankhule, Pauloyo anati, “Ine ndikudziwa kuti inu mwakhala mukuweruza dziko lino zaka zambiri, kotero ndikukondwera kuti ndikudziteteza ndekha pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 24:10
12 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;


Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?


nanena, M'mzinda mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu.


Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.


Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.


koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi chilamulo chanu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.


Ndipo anatulutsa Aleksandro m'khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Aleksandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.


Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:


ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felikisi kazembeyo.


Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:


koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;


Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa