Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 24:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Patapita masiku asanu, Ananiya, mkulu wa ansembe onse, adadza pamodzi ndi akuluakulu ena a Ayuda, ndi katswiri wina wolankhulira anthu pa milandu, dzina lake Tertulo. Iwo adafika pamaso pa bwanamkubwa uja, nayamba kuneneza Paulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Patapita masiku asanu mkulu wa ansembe Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena ndi katswiri woyankhulira anthu pa milandu wotchedwa Tertuliyo anapita ku Kaisareya ndipo anafotokoza mlandu wa Paulo kwa Bwanamkubwayo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 24:1
15 Mawu Ofanana  

Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima.


kapitao wa makumi asanu, ndi munthu wolemekezeka, ndi phungu, ndi mmisiri waluso, ndi wodziwa matsenga.


Ndipo tsiku lopangira Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.


Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye mu Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,


Ndipo mkulu wa ansembe Ananiya analamulira akuimirirako ampande pakamwa pake.


ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felikisi kazembeyo.


Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.


iwowo, m'mene anafika ku Kesareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye.


anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m'nyumba ya milandu ya Herode.


popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha chikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira;


Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,


amene ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndili ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wake.


Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda ananenera Paulo kwa iye; ndipo iwo anamdandaulira,


Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadze ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu.


Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhale ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa