Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 23:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa kubwalo la akulu a milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa kubwalo la milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Iyeyo adati, “Ayuda ena apangana zodzakupemphani kuti mupite ndi Paulo ku Bwalo lao Lalikulu lamilandu maŵa, ngati kuti iwowo akufuna kufunsitsa bwino za mlandu wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mnyamatayo anati, “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mubwere ndi Paulo ku Bwalo Lalikulu, ngati kuti akufuna kudziwa bwino za iye.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 23:20
8 Mawu Ofanana  

Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu a milandu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.


Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu a milandu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.


Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?


Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.


Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa